Genesis 17:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lomwelo Abrahamu adakumbukira zimene Mulungu adamuuza, ndipo adatenga mwana wake Ismaele ndi akapolo onse obadwira m'nyumba mwake, kapena amene Abrahamu adaŵagula, kungoti amuna onse a m'nyumba mwake, naŵaumbala monga momwe Mulungu adaamuuzira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Abrahamu anachita mdulidwe mwana wake Ismaeli ndi onse amene anali mʼbanja lake, mbadwa ngakhale kapolo ochita kugula ndi ndalama, monga mmene Mulungu analamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abrahamu anatenga Ismayeli mwana wace ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwace, ndi onse, amene anagulidwa ndi ndalama zace, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwace kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.