Genesis 17:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzina lako silidzakhalanso Abramu, koma Abrahamu. Limeneli ndilo dzina lako, chifukwa ndikukusandutsa kholo la anthu a mitundu yambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sudzachedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; cifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.