Genesis 18:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adaonekera Abrahamu ku mitengo ya thundu ya ku Mamure ija. Abrahamuyo atakhala pa khomo la hema lake nthaŵi yamasana kutatentha,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anadza kwa Abrahamu pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya ku Mamre. Abrahamu nʼkuti atakhala pansi pa khoma la tenti yake masana, dzuwa likutentha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamre, pamene anakhala pa khomo la hema wace pakutentha dzuwa.