Genesis 18:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.” Sara ankangomvetsera ali kuseri kwa chitseko cha hema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mmodzi mwa iwo anati, “Mosakayikira ndidzabweranso pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.” Koma Sara amene anali kumbuyo kwa Abrahamu pa khoma la tenti ankamva zonsezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yace; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pace.