Genesis 18:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abrahamu pamodzi ndi Sara anali nkhalamba zokhazokha, ndipo nthaŵi imeneyo nkuti Sara ataleka kusamba monga amachitira akazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, anapitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumachita ndi akazi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abrahamu ndi Sara anali okalamba kale ndipo anali ndi zaka zambiri. Sara nʼkuti atapyola kale pa msinkhu oti nʼkubereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, ana pitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumacita ndi akazi;