Genesis 18:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi pali chimene chikhoza kumukanika Yehova? Pa nthawi yake, ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzabala mwana wamwamuna.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi ciripo cinthu comlaka Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yace, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.