Genesis 18:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nanga bwanji patakhala anthu makumi asanu olungama mu mzindamo? Kodi mudzawonongadi onse osausiyako mzindawo chifukwa cha anthu makumi asanu olungama omwe ali mʼmenemo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowa cifukwa ca olungama makumi asanu ali momwemo?