Genesis 18:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga pa chiŵerengero cha 50 pakangopereŵera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asoŵa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
bwanji anthu olungama atacheperapo ndi asanu pa anthu makumi asanu? Kodi mudzawononga mzinda wonse chifukwa cha asanuwo?” Iye anati, “Nditapezamo anthu 45, sindidzawuwononga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse cifukwa ca kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.