Genesis 18:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Abrahamu adati, “Chonde ndapota nanu, musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso. Nanga mutapezeka anthu olungama 30?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu 30, sindidzauwononga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Abrahamu anati, “Pepanitu musandipsere mtima Ambuye, koma mundilole kuti ndiyankhule. Nanga mutapezekamo anthu makumi atatu okha?” Iye anayankha, “Sindidzatero ngati atapezekamo anthu makumi atatu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzacita.