Genesis 18:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine tsopano ndikatenga chakudya, kuti mukadya mupeze mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Mwabwera pakhomo panga pano, motero ndiyenera kukutumikirani.” Anthuwo adayankha kuti, “Chabwino, uchite monga waneneramo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ndikutengereniko kachakudya kuti mudye kuti mwina nʼkupezako mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Inu mwafika kumalo kwa mtumiki wanu.” Ndipo iwo anamuyankha nati, “Zikomo kwambiri, chita monga wanenera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzatenga cakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, cifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Cita comweco monga momwe wanena.