Genesis 19:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adaŵachititsa khungu anthu onse amene adaaima pabwalowo, achinyamata ndi okalamba omwe, kotero kuti sadathenso kuwona khomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, ang'ono ndi akulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anawachititsa khungu anthu amene anali panja pa nyumba aja, aangʼono ndi aakulu omwe, kuti asaone pa khomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, ang'ono ndi akuru, ndipo anabvutika kufufuza pakhomo.