Genesis 19:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Loti adapita kwa anyamata amene ankafuna kukwatira ana akewo naŵauza kuti, “Fulumirani, tiyeni tituluke kuno, chifukwa patsala pang'ono kuti Chauta aononge malo ano.” Koma iwowo ankangoyesa nthabwala chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene anakwata ana ake akazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mudziwu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka Loti nanena nao akamwini ace amene anakwata ana ace akazi, nati, Taukani, turukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mudziwu; koma akamwini ace anamyesa wongoseka.