Genesis 19:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'mamaŵa, angelo aja adayesa kumufulumizitsa Loti namuuza kuti, “Fulumira! Iweyo ndi mkazi wako ndi ana ako aakazi aŵiri, mutuluke kupita kunja kwa mzinda, kuti mupulumutse moyo wanu pamene mzinda uno ukukaonongedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako akazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmene kumacha, angelo aja anamufulumizitsa Loti nati, “Nyamuka, tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwo, ndipo mutuluke mu mzindawo kuopa kuti mungaphedwe pamodzi nawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene kunaca, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako akazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mudzi.