Genesis 19:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Loti ankakayikabe, tsono Chauta adamumvera chifundo. Motero anthuwo adatenga Loti, mkazi wake ndi ana ake aŵiri aja moŵagwira pa dzanja, naŵatulutsa mumzindamo, nkuŵasiya panja pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake akazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Loti ankakayikabe. Koma Yehova anawachitira chifundo motero kuti anthu aja anagwira mkazi wake ndi ana ake aakazi aja nawatsogolera bwinobwino kuwatulutsa mu mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anacedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lace, ndi dzanja la mkazi wace ndi dzanja la ana ace akazi awiri; cifukwa ca kumcitira cifundo Yehova; ndipo anamturutsa iye, namuika kunja kwa mudzi.