Genesis 19:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ataŵatulutsira kunja kwa mzindawo, mmodzi mwa angelowo adati, “Thamangani, mupulumutse moyo wanu. Musacheukire m'mbuyo, ndipo musaime m'chigwamo. Thaŵirani ku mapiri kuti mungaphedwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atangowatulutsa, mmodzi wa angelowo anati, “Thawani kuti mudzipulumutse, musachewuke, musayime pena paliponse mʼchigwamo! Thawirani ku mapiri kuopa kuti mungawonongeke!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene anawaturutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usaceuke, usakhale pacigwa pali ponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.