Genesis 19:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo patsidyapo pali kamzinda kakang'ono. Pamenepo mpafupi, ndingathe kukafika. Bwanji ndipite kumeneko. Nkochepa kwambiri, koma ndikhoza kupulumukirako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli waung'ono; ndithawiretu kumeneko, suli waung'ono nanga? Ndipo ndidzakhala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma, chapafupi pomwepa pali mudzi woti ndikhoza kuthamanga nʼkukafikako. Mundilole ndithawireko, ndi waungʼono kwambiri, si choncho? Mukatero, moyo wanga upulumuka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli wong'ono; ndithawiretu kumeneko, suli wong'ono nanga? ndipo ndidzakhala ndi moyo.