Genesis 19:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Fulumira! Thamanga! Sindichita kena kalikonse mpaka iwe utafika kumeneko.” Choncho Loti adathamanga nakafika ku kamzinda kaja. Nchifukwa chake kamzindako adakatcha Zowari.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mudziwo Zowari.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma uthawireko mofulumira chifukwa sindichita kena kalikonse mpaka utafikako.” (Nʼchifukwa chake mudziwo unatchedwa Zowari).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kucita kanthu usadafike kumeneko. Cifukwa cace anacha dzina la mudziwo Zoari.