Genesis 19:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero pamene Chauta ankaononga mizinda yam'chigwayo, adakumbukira pemphero la Abrahamu, ndipo adapulumutsa Loti ku chiwonongeko chimene chidasakaza mizinda ija m'mene Loti ankakhala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene Mulungu anaononga midzi ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga midzi m'mene anakhalamo Loti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Mulungu anawononga mizinda ya ku chigwa, koma anakumbukira pemphero la Abrahamu natulutsa Loti ku sulufule ndi moto zimene zinawononga mizinda ya kumene Loti amakhalako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene Mulungu anaononga midzi ya m'cigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, naturutsa Loti pakati pa cionongeko, pamene anaononga midzi m'mene anakhalamo Loti.