Genesis 19:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Loti adaumirirabe kuŵapempha, ndipo pambuyo pake iwo adavomera, napita kunyumba kwa Loti. Tsono Loti adaŵachitira phwando. Adaŵaphikira buledi wosafufumitsa naŵakonzera chakudya chokoma kwambiri, anthuwo nkudya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iye anawawumiriza kwambiri kotero kuti anapita naye pamodzi ku nyumba kwake. Anawakonzera chakudya buledi wopanda yisiti ndipo anadya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwace; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda cotupitsa, ndipo anadya,