Genesis 19:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti Loti ankaopa kukhala ku Zowari, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi aŵiri aja, adapita ku dziko lamapiri, onsewo nkumakakhala m'mapanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Loti anabwera kutuluka m'Zowari nakhala m'phiri ndi ana akazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala m'Zowari, ndipo anakhala m'phanga, iye ndi ana ake akazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Loti ndi ana ake awiri aakazi anachoka ku Zowari nakakhala ku mapiri, chifukwa amachita mantha kukhala ku Zowari. Iye ndi ana ake awiri ankakhala mʼphanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Loti anabwera kuturuka m'Zoari nakhala m'phiri ndi ana akazi awiri pamodzi naye: cifukwa anaopa kukhala m'Zoari, ndipo anakhata m'phanga, iye ndi ana ace akazi.