Genesis 19:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho usiku womwewo anawo adampatsa vinyo bambo waoyo. Zitatero, mwana wamkuluyo adagona ndi bambo wake. Pamenepo nkuti bamboyo ataledzera kwambiri, kotero kuti sankadziŵa zimene zinkachitika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wake; ndipo sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usiku umenewo analedzeretsa vinyo abambo awo, ndipo wamkuluyo analowa nagona naye. Abambo awo samadziwa kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wace; ndipo sanadziwa pomwe anagona ndi pomwe anauka,