Genesis 19:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero usiku umenewo adamledzeretsanso, ndipo mwana wamng'onoyo adagona ndi bambo wake. Nthaŵi imeneyinso nkuti bamboyo ataledzera, kotero kuti sadadziŵe zochitikazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho analedzeranso vinyo abambo awo usiku umenewonso, ndipo mwana wamkazi wamngʼono anapita nagona nawo. Abambo awo sanadziwenso kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwa pomwe anagona ndi pomwe anauka.