Genesis 19:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani, ine ndili ndi ana aakazi aŵiri, anamwali osadziŵa mwamuna. Bwanji ndikupatseni ana ameneŵa kuti muchite nawo zomwe mukufuna. Koma alendoŵa, musaŵachite kanthu kena kalikonse chifukwa ndi alendo anga, ndipo ndiyenera kuŵatchinjiriza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonanitu, ndili ndi ana akazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa chindwi langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, ine ndili ndi ana anga akazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Mundilole ndikutulutsireni amenewo ndipo muchite nawo zimene mungafune. Koma musachite chilichonse ndi anthuwa, pakuti iwowa ndi alendo anga ndipo ndiyenera kuwatchinjiriza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonanitu, ndiri ndi ana akazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwaturutsire iwo kwa inu, mucite nao comwe cikomera inu; koma anthu awa musawacitire iwo kanthu; cifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa cindwi langa,