Genesis 19:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwowo adati, “Choka apa, wakudza iwe! Ndiwe yani iwe kuti ungatiwuze zoti tichite? Tachoka apa! Mwina mwake tingathe kukuzunza kwambiri kupambana iwowo.” Motero adamkankha Lotiyo, nasendera kuti akathyole chitseko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakucitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe citseko.