Genesis 2:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kupatula mtengo wokhawo umene umadziŵitsa zabwino ndi zoipa. Zipatso za mtengo umenewo usadye. Ukadzadya, ndithu udzafa!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma usadye zipatso za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choyipa, popeza ukadzadya za mu mtengowu udzafa ndithu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa, usadye umenewo; cifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.