Genesis 2:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adatenga dothi naumba nyama zonse ndi mbalame zonse, nabwera nazo kwa Adamu kuti azitche maina. Mwakuti maina amene Adamu adazitcha, maina ake ndi omwewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazicha; ndipo maina omwe onse anazicha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika