Genesis 2:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamu adati, “Uyutu ndiye ndi fupa lochokera ku mafupa anga, mnofu wochokera ku mnofu wanga. Adzatchedwa Mkazi, chifukwa watengedwa kwa Mwamuna.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu uja anati, “Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga; adzatchedwa ‘mkazi,’ popeza wachokera mwa mwamuna.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye pfupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzachedwa Mkazi, cifukwa anamtenga mwa mwamuna.