Genesis 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, naliyeretsa, chifukwa choti pa tsiku limenelo adapuma atatsiriza zonse zimene ankachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mulungu anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri nalipatula, chifukwa pa tsiku limeneli Iye anapumula ku ntchito yonse yolenga imene anayigwira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lacisanu ndi ciwiri, naliyeretsa limenelo: cifukwa limenelo ada puma ku nchito yace yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga.