Genesis 2:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
panalibe chomera chilichonse pa dziko lapansi, ndipo mbeu zinali zisanamere, chifukwa Chauta Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Ndipo panalibenso wina aliyense wolima pa nthaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
zitsamba zinali zisanamere ndipo chomera chilichonse chinali chisanamerenso popeza Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Panalibe munthu wolima nthaka,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; cifukwa Yehova Mulungu sanabvumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka;