Genesis 20:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero pamene Mulungu adandituma kuchokera kunyumba kwa bambo wanga, kuti ndipite ku maiko achilendo, ndidaamuuza mkazi wangayu kuti, ‘Undiwonetse kuti ndiwedi wokhulupirika kwa ine, pouza aliyense kuti ndine mlongo wako, kulikonse kumene tizipita.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiye pamene Mulungu anati ndichoke ku nyumba ya abambo anga, ndinawuza mkazi wangayu kuti, ‘Kuti uwonetse kuti ndiwe mkazi wokoma mtima, uziwuza anthu kulikonse kumene tingapite kuti ndine mlongo wako.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ici ndico cokoma mtima udzandicitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, iye ndiye mlongo wanga.