Genesis 20:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adamuyankha m'maloto momwemo kuti, “Inde ndikudziŵa kuti iwe udachita zimenezi popanda mtima wako kukutsutsa. Choncho ndidakuletsa ndine kuti usandichimwire pakumkhudza mkaziyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono kumaloto komweko Mulungu anati kwa iye, “Inde ndikudziwa kuti wachita izi moona mtima, ndipo Ine sindinafune kuti undichimwire. Nʼchifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, lode ndidziwa ine, kuti wacita ico ndi mtima wangwiro, ndipo lnenso ndinakuletsa iwe kuti usandicimwire ine: cifukwa cace sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo.