Genesis 20:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano, umpereke mkazi ameneyu kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti usafe. Koma ukapanda kumpereka, ndikukuchenjezeratu kuti udzafa ndithu, iweyo ndi banja lako lonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano kabwezere mkaziyo kwa mwamuna wake. Iyeyu ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti ukhale ndi moyo. Koma ukapanda kukamupereka, udziwiretu kuti udzafa pamodzi ndi onse a pa banja pako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wace; cifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.