Genesis 20:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abimeleki adaitana Abrahamu namufunsa kuti, “Kodi iwe watichita zotani? Kodi ine ndakulakwira chiyani, kuti iweyo undiputire chilango chotere ine ndi onse a mu ufumu wanga? Zimene wandichitazi nzosayenera konse kuzichita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Abimeleki anayitana Abrahamu ndipo anati, “Kodi wachita chiyani? Ndakulakwira chiyani kuti undibweretsere ine pamodzi ndi anthu anga chilango chachikulu chotere? Wandichitira zinthu zimene sizinayenera kuchitika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abimeleke anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Waticitira ife ciani iwe? Ndakucimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga ucimo waukuru? Wandicitira ine zosayenera kuzicita.