Genesis 21:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mtima wako usavutike chifukwa cha mwanayo ndi mzikazi wako Hagara. Zonse zimene akukuuza Sara uchite, chifukwa Isakiyu ndi amene adzakhala kholo la zidzukulu zako monga momwe ndidakulonjezera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mulungu anamuwuza Abrahamu kuti, “Usamve chisoni motero ndi mnyamatayu ndi mdzakazi wakoyu. Mvetsera chilichonse chomwe Sara akukuwuza, chifukwa zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, cifukwa ca mnyamatayo, ndi cifukwa ca mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ace; cifukwa kuti mwa Isake zidzaitanidwa mbeu zako.