Genesis 21:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adapatsa Hagara chakudya ndi thumba lachikopa la madzi. Kenaka adatenga mwanayo nabereketsa Hagara, ndipo atatero adamuuza kuti azipita. Hagara adachokadi, nkumangoyendayenda m'chipululu cha Beereseba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mchenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmamawa wake, Abrahamu anatenga chakudya ndi botolo la madzi nazipereka kwa Hagara. Anasenzetsa Hagara nawaperekeza pangʼono ndi mnyamatayo. Hagara ananyamuka nayendayenda mʼchipululu cha Beeriseba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mcenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pace, ndi mwana, namcotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocerera m'cipululu ca Beereseba.