Genesis 21:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adakakhala pansi poteropo, pa mtunda wa mamita 100, chifukwa ankati, “Ine sindingathe kumaonerera mwana wanga alikufa chotere.” Ali pansi pomwepo, mwanayo adayamba kulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa muvi: chifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ake nalira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Hagara anachoka nakakhala pansi cha pakatalipo, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi, popeza mʼmaganizo mwake amati, “Sindingaonerere mwanayu akufa.” Ndipo anakhala pansi cha poteropo nʼkumalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patari, monga pakugwa mubvi: cifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ace nalira,