Genesis 21:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adamumva mwanayo akulira, ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba, adati, “Kodi iwe Hagara, chikukuvuta nchiyani? Usachite mantha. Mulungu wamva kulira kwa mwanayu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? usaope; cifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.