Genesis 21:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mulungu adatsekula maso a Hagara, ndipo adaona chitsime. Iye adapita pachitsimepo, nakadzaza thumba lachikopa lija ndi madzi, nkumwetsako mwanayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwake, ndipo anaona chitsime cha madzi; namuka nadzaza mchenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mulungu anatsekula maso a Hagara ndipo anaona chitsime cha madzi. Choncho anapita nadzaza botolo lija ndi madzi ndi kumupatsa mnyamatayo kuti amwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwace, ndipo anaona citsime ca madzi; namuka nadzaza mcenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.