Genesis 21:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imeneyo Abimeleki, pamodzi ndi Fikolo, mkulu wa gulu lake la ankhondo, adapita kwa Abrahamu kukamuuza kuti, “Inu, Mulungu ali nanu pa zonse zimene mumachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawiyo, Abimeleki ndi Fikolo wamkulu wankhondo wake anati kwa Abrahamu, “Mulungu ali nawe pa chilichonse umachita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali nthawi yomweyo. Abimeleke ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yace anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzicita iwe;