Genesis 21:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Ismaele, amene Hagara Mwejipito uja adabalira Abrahamu, ankamunyoza Isaki mwana wa Sara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Sara anaona mwana wake wamwamuna wa Hagara Mwejipito, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Sara anaona kuti mwana wamwamuna amene Hagara Mwigupto anamuberekera Abrahamu amamuseka,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sara anaona mwana wace wamwamuna wa Hagara M-aigupto, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka.