Genesis 22:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziŵa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamcitire iye kanthu; cifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.