Genesis 22:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abrahamu adaŵatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abrahamu anacha dzina lace la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova cidzaoneka.