Genesis 22:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adati, “Tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mulungu anati, “Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isake, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.