Genesis 22:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake Abrahamu adakonza chishalo pa bulu wake nadulanso nkhuni zokaotchera nsembe, ndipo adatenga Isaki pamodzi ndi antchito ake aŵiri, nanyamuka ulendo wopita ku malo amene Mulungu adaamuuza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abrahamu anadzuka mmamawa wake namangirira chokhalira pa bulu. Atadula nkhuni zokwanira zowotchera nsembe yopsereza, Abrahamu, antchito ake awiri pamodzi ndi Isake ananyamuka kupita kumalo kumene Mulungu anamuwuza Abrahamu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga buru wace, natengako anyamata ace awiri pamodzi naye, ndi Isake mwana wace, nawaza nkhuni za nsembe, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye,