Genesis 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Isaki adaitana bambo wake kuti, “Atate.” Abrahamu adavomera kuti, “Ee, mwana wanga.” Isaki adafunsa kuti, “Moto ndi nkhuni ndikuziwona, zilipo, koma nanga mwanawankhosa wokaotchera nsembe ali kuti?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Isaki ananena ndi Abrahamu atate wake, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwanawankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?” Abrahamu anayankha, “Ee mwana wanga.” Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Isake ananena ndi Abrahamu atate wace, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?