Genesis 22:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika ku malo amene adaamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye pa guwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika pamalo pamene Mulungu anamuwuza paja, Abrahamu anamangapo guwa lansembe nayika nkhuni pamwamba pa guwapo. Kenaka anamumanga mwana wake Isake namugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni paja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isake mwana wace, namuika iye pa guwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.