Genesis 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo nkuti Efuroniyo ali pamodzi ndi Ahiti ku malo ochitirako msonkhano pa chipata cha mudzi. Ndipo anthu onsewo akumva, iye adayankha kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti: ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake, kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo nʼkuti Efroni Mhiti ali pomwepo pakati pa anthuwo amene anabwera ku chipata cha mzindawo. Ndipo onse akumva anamuyankha Abrahamu
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Efroni anakhala pakati pa ana a Heti: ndipo Efroni Mhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Heti, onse amene analowa pa cipata ca mudzi wace, kuti,