Genesis 23:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ai, mbuyanga. Ine ndikupatsani munda wonsewu pamodzi ndi phanga lomweli. Ndikupatsani chabe malowo pamaso pa anthu anga onseŵa, kuti muikemo amai amene atisiyaŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nati, “Ayi mbuye wanga tandimverani, ine ndikukupatsani mundawo ndiponso phanga limene lili mʼmenemo. Ndikukupatsani malowa pamaso pa anthu a mtundu wanga. Chonde ikani mtembo wamkazi wanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga liri m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu.