Genesis 23:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nauza Efuroni pakhamu pa onse kuti, “Koma chonde, mundimvere, ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mtengo wake wa mundawu, kuti mkazi wanga ndidzamuike m'menemo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena kwa Efuroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wake wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anthu onse akumva Abrahamu anati kwa Efroni, “Ngati kungatheke, chonde ndimvereni. Ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mundawu kuti ine ndiyike mkazi wanga mʼmenemo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena kwa Efroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wace wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo.