Genesis 23:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abrahamu adavomera, ndipo pamaso pa anthu onse a ku Hiti adaŵerenga masekeli a siliva okwana 400 amene Efuroni adaatchula, potsata ndalama zomwe anthu amalonda ankagwiritsa ntchito m'dzikomo pa nthaŵi imeneyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abrahamu anavomera mtengo umene ananena Efroni Ahiti onse akumva ndipo anamuwerengera masekeli asiliva okwana 400 monga mwa mtengo wa ndalama umene amalonda a nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abrahamu anamvera Effoni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Heti, masekele a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda.